Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 47:11-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Koma pali matope ace ndi zithaphwi zace sipadzakonzeka, paperekedwa pakhale pamcere.

12. Ndipo kumtsinje, kugombe kwace tsidya lino ndi lija, kudzamera mtengo uli wonse wa cakudya, osafota tsamba lace, zipatso zace zomwe zosasowa; idzabala zipatso zatsopano mwezi ndi mwezi, popeza madzi ace atumphuka m'malo opatulika; ndi zipatso zace zidzakhala cakudya, ndi tsamba lace lakuciritsa.

13. Atero Ambuye Yehova, Malire amene mugawe nao dziko likhale colowa cao monga mwa mafuko khumi ndi awiri a Israyeli ndi awa: Yosefe akhale nao magawo awiri.

14. Ndipo mudzakhala nalo colowa canu wina ndi mnzace yemwe, ndilo limene ndinakwezapo dzanja langa kulipereka kwa makolo anu, ndi dziko ili lidzakugwerani colowa canu.

15. Ndipo malire a dzikoli ndi awa: mbali ya kumpoto, kuyambira ku nyanja yaikuru, kutsata njira ya ku Heteloni, kufikira polowera ku Zedadi;

16. Hamati, Berota, Sibraimu, ndiwo pakati pa malire a Damasiko, ndi malire a Hamati; Hazere Hatikoni ndiwo ku malire a Haurani.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 47