Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 46:14-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Uperekenso nsembe yaufa pamodzi naye m'mawa ndi m'mawa, limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, ndi limodzi la magawo atatu la hini wa mafuta, kusanganiza ndi ufa wosalala, ndiyo nsembe yaufa ya Yehova kosalekeza, mwa lemba losatha.

15. Momwemo apereke mwana wa nkhosa, ndi nsembe yaufa, ndi mafuta, m'mawa ndi m'mawa, nsembe yopsereza kosalekeza.

16. Atero Ambuye Yehova, Kalonga akapatsa mwana wace wina wamwamuna mphatso idzakhala colowa cace, ndico cao cao ca ana ace, colowa cao.

17. Koma akapatsa mphatso yotenga ku colowa cace kwa wina wa anyamata ace, idzakhala yace mpaka caka ca ufulu; pamenepo ibwerere kwa kalonga, koma colowa cace cikhale ca ana ace.

18. Ndipo kalonga asatengeko colowa ca anthu kuwazunza, ndi kulanda dziko lao lao; apatse ana ace colowa kulemba dziko lace lace, kuti anthu anga asabalalike, yense kucoka m'dziko lace.

19. Pamenepo anapita ndi ine podzera paja pali ku mbali ya cipata kumka ku zipinda zopatulika za ansembe zoloza kumpoto; ndipo taonani, kunali malo cauko kumadzulo.

20. Ndipo anati kwa ine, Pano ndipo ansembe aziphikira nsembe yoparamula, ndi nsembe yaucimo; kumenenso azioca mikate ya ufa wa nsembe, kuti asaturuke nazo ku bwalo lakunja ndi kupatulikitsa anthu,

21. Pamenepo anaturukira nane ku bwalo lakunja, nandipititsa ku ngondya zinai za bwaloli; ndipo taonani, m'ngondya monse munali bwalo.

22. M'ngondya zinai za bwalo munali mabwalo ocingika, m'litali mwace mikono makumi anai, kupingasa kwace makumi atatu; awa anai m'ngondyazi analingana muyeso wace.

23. Ndipo panali maguwa pozungulira pace m'menemo, pozungulira pace pa mabwalo anai; ndipo anamanga maguwawo ndi mafuwa pansi pace pozungulirapo.

24. Ndipo anati kwa ine, Izi ndi nyumba zophikiramo, kumene atumiki a kacisi aziphikira nsembe ya anthu.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 46