Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 46:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Atero Ambuye Yehova, Pa cipata ca bwalo lam'kati coloza kum'mawa patsekedwe masiku asanu ndi limodzi ogwira nchito; koma tsiku la Sabata patsegulidwe, ndi tsiku lokhala mwezi patsegulidwe.

2. Ndipo kalonga azilowera njira ya ku khonde la cipataco, kunja kwace, naime ku nsanamira ya cipata; ndipo ansembe akonze nsembe yace yopsereza, ndi nsembe zace zoyamika, nalambire iye ku ciundo ca cipata; atatero aturuke; koma pacipata pasatsekedwe mpaka madzulo.

3. Ndipo anthu a m'dziko alambire pa citseko ca cipata ici pamaso pa Yehova pamasabata, ndi pokhala mwezi.

4. Ndipo nsembe yopsereza imene kalonga azipereka kwa Yehova pa Sabata ndiyo ana a nkhosa asanu ndi mmodzi opanda cirema, ndi nkhosa yamphongo yopanda cirema,

5. ndi nsembe yaufa ikhale efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi nsembe ya ufa wa pa ana a nkhosa, monga akhoza kupatsa; ndi hini a wa mafuta wa paefa.

6. Ndipo nsembe ya tsiku lokhala mwezi ikhale mwana wa ng'ombe wopanda cirema, ndi ana a nkhosa asanu ndi mmodzi, ndi nkhosa yamphongo, zikhale zopanda cirema;

7. ndipo akonze nsembe yaufa, efa wa pa ng'ombe, ndi efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi pa ana a nkhosa, monga akhoza; ndi hini wa mafuta wa paefa.

8. Ndipo polowa kalonga azilowera njira ya ku khonde la cipata, naturuke njira yomweyo.

9. Koma pofika anthu a m'dziko pamaso pa Yehova m'madyerero oikika, iye amene alowera njira ya ku cipata ca kumpoto kudzalambira, aturukire njira ya ku cipata ca kumwera; ndi iye amene alowera njira ya ku cipata ca kumwera, aturukire njira ya ku cipata ca kumpoto; asabwerere njira ya cipata anadzeraco, koma aturukire m'tsogolo mwace.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 46