Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 43:17-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndi phaka, m'litali mwace mikono khumi ndi inai, ndi kupingasa kwace mikono khumi ndi inai ku mbali zace zinai; ndi mkuzi wace pozungulira pace mkono wa nusu, ndi tsinde lace mkono pozungulira pace, ndi makwerero ace aloza kum'mawa.

18. Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, atero Ambuye Yehova, Malemba a guwa la nsembe, tsiku lakulimanga, kuperekapo nsembe zopsereza, ndi kuwazapo mwazi, ndi awa;

19. Upatse ansembe Alevi, a mbeu ya Zadoki, okhala pafupi ndi Ine, kunditumikira Ine, ati Ambuye Yehova, mwana wa ng'ombe, akhale wa nsembe yaucimo.

20. Nutengeko mwazi wace, ndi kupaka pa nyanga zinai za guwa, ndi pa ngondya zinai za phaka, ndi pa mkuzi wace pozungulira; motero uliyeretse ndi kulicitira cotetezera.

21. Utengenso ng'ombe ya nsembe yaucimo, aipsereze pa malo oikika a kacisi kunja kwa malo opatulika.

22. Ndipo tsiku laciwiri upereke tonde wopanda cirema, akhale nsembe yaucimo; ndipo ayeretse guwa la nsembe monga umo analiyeretsera ndi ng'ombeyo.

23. Utatha kuliyeretsa upereke mwana wa ng'ombe wopanda cirema, ndi nkhosa yamphongo ya zoweta yopanda cirema.

24. Ndipo ubwere nazo kwa Yehova, ndi ansembe athirepo mcere, ndi kuzipereka nsembe yopsereza ya Yehova.

25. Masiku asanu ndi awiri uzikonzera mbuzi tsiku ndi tsiku, ikhale nsembe yaucimo; akonzerenso mwana wa ng'ombe, ndi nkhosa yamphongo ya zoweta zopanda cirema.

26. Masiku asanu ndi awiri acite cotetezera guwali ndi kuliyeretsa, momwemo alipatule.

27. Ndipo atatsiriza masiku, kudzacitika tsiku lacisanu ndi citatu ndi m'tsogolo, ansembe azicita nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zoyamika pa guwalo; ndipo ndidzakulandirani, ati Ambuye Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 43