Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 42:3-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Pandunji pa mikono makumi awiri a bwalo lam'kati, ndi pandunji pa moyalamo mwa miyala, mwa bwalo lakunja, panali khonde lam'mwamba, lokomana ndi khonde linzace losanjikika paciwiri.

4. Ndi kukhomo kwa zipinda anakonza poyendapo, kupingasa kwace mikono khumi m'kati mwace, njira ya mikono zana limodzi, ndi makomo ao analoza kumpoto.

5. Ndipo zipinda zapamwamba zinacepa, pakuti makonde am'mwamba analanda pamenepo, cifukwa cace zinacepa koposa zapansi ndi zapakati m'nyumba yazipinda.

6. Pakuti zinasanjikizana pawiri, ndipo zinalibe nsanamira ngati nsanamira za kumabwalo; cifukwa cace zam'mwambazo zinacepa koposa zakunsi ndi zapakati kuyambira pansi.

7. Ndipo linga linali kunialo, loli'ngana ndi nyumba yazipinda, kuloza ku bwalo lakunja, popenyana ndi nyumba yazipinda, m'litali mwace munali mikono makumi asanu.

8. Pakuti kupingasa kwace kwa nyumba yazipinda inali m'bwalo lakunja, kunali mikono makumi asanu; ndipo taonani, kuloza ku khomo la Kacisi inali mikono zana limodzi.

9. Ndipo pansi pa zipinda izi panali polowera mbali ya kum'mawa, poloweramo kucoka ku bwalo lakunja.

10. M'kucindikira kwa linga la bwalo, kuloza kumwera, cakuno ca mpatawo, cakuno ca nyumba, panali nyumba yazipinda.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 42