Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 41:11-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndi makomo a zipinda za m'mphepete analoza kumpatawo, khomo lina kumpoto, ndi lina kumwela; ndi malo a pa mpatawo anayesa mikono isanu kupingasa kwace pozungulira pace.

12. Ndipo nyumba inali kutsogolo kwa mpata wa mbali ya kumadzulo inali ya mikono makumi asanu ndi awiri kupingasa kwace; ndi khoma la nyumbayo pozungulira pace linali la mikono isanu kucindikira kwace; ndi m'litali mwace mikono makumi asanu ndi anai.

13. Momwemo anayesa kacisi m'litali mwace mikono zana limodzi; ndi mpatawo, ndi nyumbayo, ndi makoma ace, mikono zana limodzi;

14. kupingasa kwace komwe kwa kukhomo kwa nyumba, ndi ku mpatawo kum'mawa, mikono zana limodzi.

15. Momwemo anayesa m'litali mwace nyumbayo inali kutsogolo kwace kwa mpata wokhala cakuno cace, ndi makonde ace am'mwamba, cakuno ndi cauko, mikono zana limodzi, ndi Kacisi wa m'katimo, ndi makonde a kubwalo;

16. ziundo, ndi mazenera a made okhazikika, ndi makonde am'mwamba akuzinga zipinda zosanjikizana zao zitatu, pandunji pa ciundo, ocinga ndi matabwa pozungulira pace, kuyambira pansi kufikira kumazenera; koma mazenera anaphimbika;

17. kufikira pamwamba pa khomo, mpaka nyumba ya m'katimo, ndi kunja kwace, ndi khoma lonse kwete m'kati ndi kunja, monga mwa miyeso.

18. Ndipo panalembedwapo ndi akerubi ndi akanjedza, kanjedza pakati pa akerubi; ndi kerubi ali yense anali ndi nkhope zace ziwiri;

19. nkhope ya munthu kuloza kukanjedza cakuno, ndi nkhope ya mwana wa mkango kuloza kukanjedza cauko, momwemo m'nyumba monse pozungulira pace.

20. Kuyambira pansi kufikira pamwamba pa khomo panalembedwa akerubi ndi akanjedza; linatero khoma la Kacisi.

21. Mphuthu za Kacisi zinali zamphwamphwa, ndi maonekedwe a pakhomo pa malo opatulika ananga maonekedwe a kacisi.

22. Guwa la nsembe linali lamtengo, msinkhu wace mikono itatu, ndi m'litali mwace mikono iwiri, ndi ngondya zace, ndi tsinde lace, ndi: thupi, nza mtengo; ndipo ananena ndi ine, Ili ndiko gome liri pamaso pa Yehova.

23. Ndipo Kacisi ndi malo opatulikitsa anali nazo zitseko ziwiri.

24. Ndipo pamakomopo panali zitseko zopatukana zotembenuzika, cina copatukana pa khomo lina cina pa linzace.

25. Ndipo panalembedwa pamenepo pa Izitseko za Kacisi akerubi ndi akanjedza, akunga aja adalembedwa pamakhoma; ndipo panali matabwa ocindikira pakhomo pakhonde panja,

26. Ndipo panali mazenera a made okhazikika, ndi akanjedza cakuno ndi cauko, kumbali zace za khonde; momwemonso pa zipinda za m'mphepete mwa nyumba, ndi pa matabwa ocindikira.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 41