Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 40:26-39 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Ndipo panali makwerero asanu ndi awiri okwererapo, ndi zidundumwa zace kumaso kwace; ndi pa nsanamira zace cakuno ndi cauko panali akanjedza.

27. Ndipo panali cipata ca bwalo lam'kati cakulozakumwela, nayesa kuyambira kucipata kufikira kucipata kumwela mikono zana.

28. Pamenepo analowa nane pa cipata ca kumwela m'bwalo lam'kati, nayesa cipata ca kumwera, monga mwa miyeso yomweyi;

29. ndi zipinda zace, ndi makhoma a pakati pace, ndi zidundumwa zace, monga mwa miyeso yomweyi; ndimo munali mazenera m'menemo, ndi m'zidundumwa zace pozungulirapo; m'litali mwace mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri mphambu isanu.

30. Ndipo panali zidundumwa pozungulirapo, m'litali mwace mikono makumi awiri mphambu isanu, ndi kupingasa kwace mikono isanu.

31. Ndi zidundumwa zace zinaloza ku bwalo lakunja, ndi pa nsanamira zace panali akanjedza, ndi pokwererapo panali makwerero asanu ndi atatu.

32. Ndipo analowa ndine m'bwalo lam'kati kuloza kum'mawa, nayesa cipata ca kum'mawa monga mwa miyeso yomweyi;

33. ndi zipindazace, ndi makhoma a pakati pace, Indi zikundumwa zace, monga mwa miyeso yomweyi; ndimo munali mazenera m'menemo, ndi m'zidundumwa zace pozungulirapo, m'litali mwace mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri mphambu isanu.

34. Ndi zidundumwa zace zinaloza ku bwalo lakunja; ndi pa nsanamira zace panali akanjedza cakuno ndi cauko; ndipo pokwerera pace panali makwerero asanu ndi atatu.

35. Pamenepo anabwera nane ku cipata ca kumpoto, naciyesa monga mwa miyeso yomweyi;

36. zipinda zace, makhoma a pakati pace, ndi zidundumwa zace; ndimo munali mazenera m'menemo pozungulirapo, m'litali mwace mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri mphambu isanu.

37. Ndi nsanamira zace zinaloza ku bwalo lakunja; ndi pa nsanamira zace panali akanjedza cakuno ndi cauko; ndipo pokwerera pace panali makwerero asanu ndi atatu.

38. Ndipo pa nsanamira za pazipata panali kanyumba ndi citseko cace; pamenepo anatsuka nsembe vopsereza.

39. Ndipo m'khonde la pacipata munali magome awiri cakuno, ndi magome awiri cauko, kuti apherepo nsembe yopsereza, ndi nsembe yaucimo, ndi nsembe yoparamula.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 40