Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 40:18-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo moyalidwamo munali pa mbali ya zipata molingana ndi utali wace wa zipata, ndimo moyalidwa mwamunsi.

19. Pamenepo anayesa kupingasa kwace kuyambira pakhomo pace pacipata cakunsi, kufikira kumaso kwace kwa bwalo la m'kati kunja kwace, mikono zana kum'mawa, ndi kumpoto.

20. Ndi cipata ca bwalo lakunja coloza kumpoto anaciyesa m'litali mwace, ndi kupingasa kwace.

21. Ndi zipinda zace ndizo zitatu cakuno, ndi zitatu cauko, ndi makhoma a pakati pace; ndi zidundumwa zace zinali monga mwa muyeso wa cipata coyambaco, m'litali mwace mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri mphambu isanu.

22. Ndi mazenera ace, ndi zidundumwa zace, ndi akanjedza ace, anali monga mwa muyeso wa cipata coloza kum'mawa; ndipo anakwerako ndi makwerero asanu ndi awiri, ndi zidundumwa zace zinali pakhomo.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 40