Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 40:1-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Caka ca makumi awiri ndi zisanu ca undende wathu, poyamba caka, tsiku lakhumi lamwezi, caka cakhumi ndi zinai atakantha mudziwo, tsiku lomwelo, dzanja la Mulungu linandikhalira; ndipo anamuka nane komweko.

2. M'masomphenya a Mulungu Iye anabwera nane m'dziko la Israyeli, nandikhalitsa pa phiri lalitali ndithu; pamenepo panali ngati mamangidwe a mudzi kumwela,

3. Ndipo anamuka nane komweko, ndipo taona, panali munthu, maonekedwe ace ngati amkuwa, ndi cingwe cabwazi m'dzanja lace, ndi bango loyesa nalo, naima kucipata iye.

4. Ndipo munthuyu anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, penya ndi maso ako, imva m'makutu mwako, nuike mtima wako pa zonse ndidzakuonetsa iwe; pakuti unatengedwa kudza kuno, kuti ndikuonetse izi; fotokozera nyumba ya Israyeli zonse uziona.

5. Ndipo taonani, panali linga kunja kwace kwa nyumba ya kacisi poizinga, ndi m'dzanja lace la munthuyo bango loyesa nalo la mikono isanu ndi umodzi, mkono uli wonse mkono kudza cikhato; ndipo anayesa cimangidweco kucindikira kwace bango limodzi, ndi msinkhu wace bango limodzi.

6. Pamenepo anafika ku cipata coloza kum'mawa, nakwera pa makwerero ace; ndipo anayesa ciundo ca cipata, bango limodzi kucindikira kwace; ndico ciundo coyamba, bango limodzi.

7. Ndi cipinda ca alonda, conse nca bango limodzi m'litali mwace, ndi bango limodzi kupingasa kwace, ndi pakati pa zipinda za alonda mikono isanu, ndi ciundo ca cipata ku mbali ya ku khonde la kucipata m'katimo, bango limodzi.

8. Anayesanso khonde la kucipata ku mbali ya kukacisi, bango limodzi.

9. Pamenepo anayesa khonde la kucipata mikono isanu ndi itatu, ndi mphuthu zace mikono iwiri; ndi khonde la kucipata linaloza kukacisi.

10. Ndi zipinda za alonda za ku cipata ca kum'mawa ndizo zitatu cakuno, ndi zitatu cauko, zitatuzi nza muyeso umodzimodzi, ndi mphuthuzo nza muyeso umodzimodzi, cakuno ndi cauko.

11. Ndipo anayesa kupingasa kwa cipata pakhoma pace mikono khumi, ndi utali wace wa cipata mikono khumi ndi itatu;

12. ndi pakhomo pa zipinda za alonda panali kakhoma ka mkono umodzi cakuno, ndi kakhoma ka mkono umodzi cauko; ndi zipinda za alonda mikono isanu ndi umodzi cakuno, ndi mikono isanu ndi umodzi cauko.

13. Ndipo anayesa cipata kuyambira ku tsindwi la cipinda ca alonda cimodzi, kufikira ku tsindwi la cinzace, kupingasa kwace ndiko mikono makumi awiri ndi isanu; makomo napenyana.

14. Anamanganso nsaaamira za mikono makumi asanu ndi limodzi; ndi bwalo la pakati pa cipata lidafikira kunsanamira.

15. Ndipo kuyambira pa khomo lolowera la cipata kufikira khomo la khonde la cipata m'katimo ndiko mikono makumi asanu.

16. Ndipo panali mazenera a made okhazikika pazipinda ndi m'makhoma a pakati pao, m'kati mwa cipata pozungulira ponse; momwemonso pazidundumwa; ndipo panali mazenera pozungulira ponse m'katimo, pa nsanamirazo panali akanjedza.

17. Pamenepo analowa nane ku bwalo lakunja, ndipo taonani, panali zipinda, ndi moyalidwa miyala mokonzekera bwalo pozungulira ponse; moyalidwa miyalamo munali zipinda makumi atatu.

18. Ndipo moyalidwamo munali pa mbali ya zipata molingana ndi utali wace wa zipata, ndimo moyalidwa mwamunsi.

19. Pamenepo anayesa kupingasa kwace kuyambira pakhomo pace pacipata cakunsi, kufikira kumaso kwace kwa bwalo la m'kati kunja kwace, mikono zana kum'mawa, ndi kumpoto.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 40