Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 4:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, dzitengere njerwa, nulike pamaso pako, nulembepo mudzi, ndiwo Yerusalemu;

2. nuuzinge, nuumangire nsanja zouzinga, nuundire nthumbira, ndi kuumangira misasa, nuuikire zogumulira pozungulira pace.

3. Nudzitengere ciwaya cacitsulo, ndi kuciika ngati khoma lacitsulo pakati pa iwe ndi mudziwo; nuulozetsere nkhope yako kuti umangidwire misasa, ndipo udzamangira misasa. Ici cikhale cizindikilo ca nyumba ya Israyeli.

4. Ndipo iwe ugonere pansi mbali yako ya kumanzere, nuikepo mphulupulu ya nyumba ya Israyeli; monga mwa kuwerenga kwa masiku amene udzagonapo udzasenza mphulupulu yao.

5. Ndipo Ine ndakuikira zaka za mphulupulu yao ngati masiku, ndiwo masiku mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai, kuti usenze mphulupulu ya nyumba ya Israyeli.

6. Ndipo utatsiriza awa, ugonerenso mbali yako ya kumanja, ndi kusenza mphulupulu ya nyumba ya Yuda; ndakuikira masiku makumi anai, kuliyesa tsiku limodzi ngati caka cimodzi.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 4