Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 38:15-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo udzaturuka m'malo mwako m'malekezero a kumpoto, iwe ndi mitundu yambiri ya anthu pamodzi ndi iwe, onsewo apakavalo, msonkhano waukuru ndi nkhondo yaikuru;

16. ndipo udzakwerera anthu anga Israyeli ngati mtambo wakuphimba dziko; kudzacitika masiku otsiriza ndidzabwera nawe ulimbane nalo dziko langa, kuti amitundu andidziwe, pozindikiridwa Ine woyera mwa iwe, Gogi, pamaso pao.

17. Atero Ambuye Yehova, Kodi iwe ndiwe iye amene ndinanena za iye masiku akale mwa atumiki anga aneneri a Israyeli, akunenera masiku aja za zaka za m'tsogolo, kuti ndidzabwera nawe kulimbana nao?

18. Ndipo kudzacitika tsiku ilo, tsiku loti Gogi adzadza kulimbana ndi dziko la Israyeli, ati Ambuye Yehova, ukali wanga udzakwera m'mphuno mwanga.

19. Pakuti ndanena mu nsanje yanga, ndi m'moto wa kuzaza kwanga, Zoonadi tsiku ilo kudzakhala kugwedezeka kwakukuru m'dziko la Israyeli;

20. motero kuti nsomba za m'nyanja, ndi mbalame za m'mlengalenga, ndi nyama za kuthengo, ndi zokwawa zonse zakukwawa pansi, ndi anthu onse akukhala padziko, zidzanjenjemera pamaso panga; ndi mapiri adzagwetsedwa, ndi potsetsereka padzagumuka, ndi makoma onse adzagwa pansi.

21. Ndipo ndidzamuitanira lupanga ku mapiri anga onse, ati Ambuye Yehova, munthu ali yense lupanga lace lidzaombana nalo la mbale wace.

22. Ndipo ndidzalimbana naye ndi mliri ndi mwazi; ndipo ndidzambvumbitsira iye, ndi magulu ace, ndi mitundu yambiri ya anthu okhala naye mbvumbi waukuru, ndi matalala akuru, moto ndi sulfure.

23. Momwemo ndidzadzikuzitsa, ndi kudzizindikiritsa woyera, ndipo ndidzadziwika pamaso pa amitundu ambiri; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 38