Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 35:8-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo ndidzadzaza mapiri ace ndi ophedwa ace pa zitunda zako, ndi m'zigwa zako, ndi m'mitsinje mwako monse; adzagwa ophedwa ndi lupanga.

9. Ndidzakusandutsa mabwinja osatha; ndi m'midzi mwako simudzakhalanso anthu; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova,

10. Popeza wanena, Mitundu iwiri iyi ya anthu ndi maiko awiri awa adzakhala anga, tidzakhala nao ngati colowa cathu, angakhale Yehova anali komweko;

11. cifukwa cace, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, ndidzacita monga mwa mkwiyo wako, ndi monga mwa nsanje yako unacita nayo pa kukwiya nao iwe; ndipo ndidzadziwika nao pamene ndikuweruza.

12. Ndipo udzadziwa kuti Ine Yehova ndidamva zamwano zako zonse udazinena pa mapiri a Israyeli, ndi kuti, Apasuka, apatsidwa kwa ife tiwadye.

13. Ndipo pakamwa panu mwadzikuza pa Ine, ndi kundicurukitsira mau anu ndawamva Ine.

14. Atero Ambuye Yehova, Pokondwerera dziko lonse ndidzakusanduliza lacipululu.

15. Monga momwe unakondwerera colowa ca nyumba ya Israyeli, papeza cidapasuka, momwemo ndidzakucitira iwe; udzakhala wopasuka, phiri la Seiri iwe, ndi Edomu lonse lonseli; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 35