Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 34:8-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Pali ine, ati Ambuye Yehova, zedi, popeza nkhosa zanga zinakhala nyama, ndi nkhosa zanga zinakhala cakudya ca zirombo zonse za kuthengo, cifukwa kunalibe mbusa, ndi abusa anga sanafunafuna nkhosa zanga, koma abusawo anadzidyetsa okha, osadyetsa nkhosa zanga;

9. cifukwa cace, abusa inu, imvani mau a Yehova:

10. Atero Ambuye Yehova, Taonani, Ine ndiipidwa nao abusa, ndidzafunsa nkhosa zanga pa dzanja lao, ndi kuwaletsa asadyetsenso nkhosazo, ngakhale kudzidyetsa okha sadzacitanso; ndipo ndidzalanditsa nkhosa zanga pakamwa pao, zisakhale cakudya cao.

11. Pakuti atero Ambuye Yehova, Taonani, Ine, Inedi ndidzapwaira nkhosa zanga ndi kuzifunafuna.

12. Monga mbusa afunafuna nkhosa zace tsiku lokhala iye pakati pa nkhosa zace zobalalika, mamwemo ndidzafunafuna nkhosa zanga; ndipo ndidzawalanditsa m'malo monse anabalalikamo tsiku la mitambo ndi la mdima.

13. Ndipo ndidzaziturutsa mwa mitundu ya anthu, ndi kuzisonkhanitsa m'maiko, ndi kulowa nazo m'dziko lao; ndipo ndidzazidyetsa pa mapiri a Israyeli, patimitsinje, ndi ponse pokhala anthu m'dziko.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 34