Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 34:15-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ine ndekha ndidzadyetsa nkhosa zanga, ndi kuzigonetsa, ati Ambuye Yehova.

16. Ndidzafuna yotayika, ndi kubweza yopitikitsidwa, ndi kulukira chika yotyoka mwendo, ndi kulimbitsa yodwalayo; koma yanenepa ndi yolimba ndidzaziononga, ndidzazidyetsa ndi ciweruzo.

17. Ndipo inu, gulu langa, atero Ambuye Yehova, ndiweruza pakati pa zoweta ndi zoweta, nkhosa zamphongo ndi atonde.

18. Kodi cikuceperani, kuti mwadya podyetsa pabwino? muyenera kodi kupondereza ndi mapazi anu podyera panu potsala? muyenera kumwa madzi ndikha, ndi kubvundulira otsalawo ndi mapazi anu?

19. Ndi nkhosa zanga zidye kodi zoponderezeka ndi mapazi anu, ndi kumwa zobvunduliridwa ndi mapazi anu?

20. Cifukwa cace atero nao Ambuye Yehova, Taonani, Ine, Inedi ndidzaweruza pakati pa zoweta zonenepa, ndi zoweta zoonda.

21. Popeza mukankha ndi nthiti ndi phewa, nimugunda zodwala zonse ndi nyanga zanu, mpaka mwazibalalitsa kubwalo,

22. cifukwa cace ndidzapulumutsa gulu langa lisakhalenso cakudya; ndipo ndidzaweruza pakati pa zoweta ndi zoweta.

23. Ndipo ndidzaziutsira mbusa mmodzi; iye adzazidyetsa, ndiye mtumiki wanga Davide, iye adzazidyetsa, nadzakhala mbusa wao.

24. Ndipo Ine Yehova ndidzakhala Mulungu wao, ndi mtumiki wanga Davide kalonga pakati pao; Ine Yehova ndanena.

25. Ndipo ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndi kuleketsa zirombo zoipa m'dzikomo; ndipo zidzakhala mosatekeseka m'cipululu, ndi kugona kunkhalango.

26. Pakuti ndidzaika izi ndi miraga yozungulira citunda canga; zikhale mdalitso; ndipo ndidzabvumbitsa mibvumbi m'nyengo yace, padzakhala mibvumbi ya madalitso.

27. Ndi mitengo ya kuthengo idzapereka zobala zao, ndi nthaka idzapereka zipatso zace, ndipo adzakhazikika m'dziko mwao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, nditadula zomangira goli lao, ndi kuwalanditsa m'manja mwa iwo akuwatumikiritsa.

28. Ndipo sadzakhalanso cakudya ca amitundu, ndi cirombo ca kuthengo sicidzawadyanso; koma adzakhala osatekeseka, opanda wina wakuwaopsa.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 34