Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 33:23-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

24. Wobadwa ndi munthu iwe, iwo okhala ku mabwinja a dziko la Israyeli anena, ndi kuti, Abrahamu anali yekha, nakhala nalo dziko colowa cace; koma ife ndife ambiri, dzikoli lipatsidwa kwa ife colowa cathu.

25. Cifukwa cace unene nao, Atero Ambuye Yehova, Mumadyera kumodzi ndi mwazi, mumakwezera maso anu ku mafano anu, ndi kukhetsa mwazi; ndipo kodi mudzakhala nalo dziko colowa canu?

26. Mumatama lupanga lanu, mumacita conyansa, mumaipsa yense mkazi wa mnansi wace; ndipo kodi mudzakhala nalo dziko colowa canu?

27. Uzitero nao, Atero Ambuye Yehova, Pali Ine, iwo okhala kumabwinja adzagwadi ndi lupanga, ndi iye ali kuthengo koyera ndidzampereka kwa zirombo, adyedwe nazo; ndi iwo okhala m'malinga ndi m'mapanga adzafa ndi mliri.

28. Ndipo ndidzasanduliza dziko likhale lacipululu ndi lodabwitsa, ndi mphamvu yace yodzikuza idzatha, ndi mapiri a Israyeli adzakhala acipululu, osapitako munthu.

29. Pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, posanduliza Ine dziko likhale lacipululu ndi lodabwitsa, cifukwa ca zonyansa zao zonse anazicita.

30. Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, ana a anthu a mtundu wako anena za iwe ku makoma ndi ku makomo a nyumba zao, nanenana yense ndi mbale wace, ndi kuti, Tiyeni tikamve mau ofuma kwa Yehova.

31. Ndipo akudzera monga amadzera anthu, nakhala pansi pamaso pako ngati anthu anga, namva mau ako, koma osawacita; pakuti pakamwa pao anena mwacikondi, koma mtima wao utsata phindu lao.

32. Ndipo taona, akuyesa iwe ngati nyimbo yacikondi ya woyimba bwino, woyimba limba bwino; pakuti akumva mau ako, koma osawacita.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 33