Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 32:25-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Pakati pa ophedwa anamuikira kama, iye ndi aunyinji ace onse, manda ace amzinga, onsewo osadulidwa, ophedwa ndi lupanga, pakuti anaopsetsa m'dziko la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje, aikidwa pakati pa ophedwa,

26. Meseke, Tubala, ndi aunyinji ace onse ali komweko, manda ace amzinga; onsewo osadulidwa, ophedwa ndi lupanga; pakuti anaopsetsa m'dziko la amoyo.

27. Koma sagona pamodzi ndi amphamvu osadulidwa adagwawo amene anatsikira kumanda ndi zida zao za nkhondo, amene anawatsamiritsa malupanga ao; ndi mphulupulu zao ziri pa mafupa ao; pakuti anaopsetsa amphamvu m'dziko la amoyo.

28. Ndipo udzatyoledwa pakati pa osadulidwa, nudzagona pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga.

29. Edomu ali komwe, mafumu ace ndi akalonga ace onse, amene anaikidwa mu mphamvu yao, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga; agona pamodzi ndi osadulidwa, ndi iwo akutsikira kudzenje.

30. Akalonga a kumpoto ali komwe onsewo, ndi Azidoni onse, amene anatsikira pamodzi ndi ophedwa, nacita manyazi cifukwa ca kuopsetsa anacititsaku ndi mphamvu yao, nagona osadulidwa pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga, nasenza manyazi ao pamodzi ndi iwo otsikira kudzenje.

31. Farao adzawaona, nadzasangalala nao aunyinji ace onse, Farao ndi ankhondo ace onse ophedwa ndi lupanga, ati Ambuye Yehova.

32. Pakuti ndinaika kuopsa kwace m'dziko la amoyo; ndipo adzaikidwa pakati pa osadulidwa, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga, ndiye Farao ndi aunyinji ace onse, ali Ambuye Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 32