Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 3:21-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Koma ukamcenjeza wolungamayo, kuti asacimwe wolungamayo, ndipo sacimwa, adzakhala ndi moyo ndithu, popeza anacenjezedwa; ndipo iwe walanditsa moyo wako.

22. Ndipo dzanja la Yehova linandikhalira komweko, nati kwa ine, Nyamuka, turuka kumka kucidikha, ndipo pomwepo ndidzalankhula ndi iwe.

23. Ndipo ndinauka ndi kuturuka kumka kucidikha, ndipo taonani, ulemerero wa Yehova unaimako monga ulemerero uja ndinauona ku mtsinje Kebara, ndipo ndinagwa nkhope pansi.

24. Pamenepo unandilowa mzimu ndi kundiimika ndikhale ciriri; ndipo analankhula ndi ine, nanena nane, Muka, katsekedwe m'nyumba mwako.

25. Koma iwe wobadwa ndi munthu, taona, adzakuikira iwe zingwe zolimba, nadzakumanga nazo, ndipo sudzaturuka pakati pao;

26. ndipo ndidzamamatiritsa lilime lako ku malakalaka ako, kuti ukhale wosanena, wosawakhalira wakuwadzudzula; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.

27. Koma pamene ndilankhula nawe ndidzatsegula pakamwa pako, nudzanena nao, Atero Yehova Mulungu. Wakumvera amvere, wasafuna kumvera akhale; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 3