Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 3:14-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. M'mwemo mzimu unandinyamula ndi kucoka nane; ndipo ndinamuka wowawidwa, womyuka mtima; koma dzanja la Yehova linandigwirizitsa,

15. Ndipo ndinafika kwa andende ku Telabibu, okhala kumtsinje Kebara, ndiko kwao; ndipo ndinakhalako woda bwa pakati pao masiku asanu ndi awiri.

16. Ndipo kunali atatha masiku asanu ndi awiri, mau a Yehova anandidzera, ndi kuti,

17. Wobadwa ndi munthu iwe, ndakuika ukhale mlonda wa nyumba ya Israyeli, m'mwemo mvera mau oturuka m'kamwa mwanga, nundicenjezere iwo.

18. Ndikanena kwa woipa, Udzafa ndithu, koma iwe osamcenjeza, wosanena kumcenjeza woipayo aleke njira yace yoipa, kumsunga ndi moyo, woipa yemweyo adzafa mu mphulupulu yace; koma mwazi wace ndidzaufuna pa dzanja lako.

19. Koma ukacenjeza woipa, osabwerera iye kuleka coipa cace kapena njira yace yoipa, adzafa mu mphulupulu yace; koma iwe walanditsamoyo wako.

20. Momwemonso akabwerera wolungama kuleka cilungamo cace, ndi kucita cosalungama, ndipo ndikamuikira comkhumudwitsa, adzafa; popeza sunamcenjeza, adzafa m'cimo lace, ndi zolungama zace adazicita sizidzakumbukika; koma mwazi wace ndidzaufuna pa dzanja lako.

21. Koma ukamcenjeza wolungamayo, kuti asacimwe wolungamayo, ndipo sacimwa, adzakhala ndi moyo ndithu, popeza anacenjezedwa; ndipo iwe walanditsa moyo wako.

22. Ndipo dzanja la Yehova linandikhalira komweko, nati kwa ine, Nyamuka, turuka kumka kucidikha, ndipo pomwepo ndidzalankhula ndi iwe.

23. Ndipo ndinauka ndi kuturuka kumka kucidikha, ndipo taonani, ulemerero wa Yehova unaimako monga ulemerero uja ndinauona ku mtsinje Kebara, ndipo ndinagwa nkhope pansi.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 3