Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 3:1-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ananena nane, Wobadwa ndi munthu iwe, Idya cimene wacipeza; idya mpukutu uwu, numuke ndi kunena ndi nyumba ya Israyeli.

2. Pamenepo ndinatsegula pakamwa panga ndipo anandidyetsa mpukutuwo.

3. Nati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, dyetsa m'mimba mwako, nudzaze matumbo ako ndi mpukutu uwu ndakupatsawu. M'mwemo ndinaudya, ndi m'kamwa mwanga munazuna ngati uci.

4. Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, Muka, nufike kwa nyumba ya Israyeli, nunene nao mau anga.

5. Pakuti sutumizidwa kwa anthu a cinenedwe cosamveka ndi cobvuta, koma kwa nyumba ya Israyeli;

6. si kwa mitundu yambiri ya anthu a cinenedwe cosamveka ndi cobvuta, amene sukhoza kudziwitsa cinenedwe cao. Zedi ndikakutumiza kwa iwowa adzamvera iwe.

7. Koma nyumba ya Israyeli siidzakumvera, pakuti siifuna kundimvera Ine; pakuti nyumba yonse ya Israyeli ndiyo yolimba mutu ndi youma mtima.

8. Taona ndakhwimitsa nkhope yako itsutsane nazo nkhope zao; ndalimbitsanso mutu wako utsutsane nayo mitu yao.

9. Ndalimbitsa mutu wako woposa mwala wolimbitsitsa, usawaopa kapena kutenga nkhawa pamaso pao; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.

10. Ananenanso nane, Wobadwa ndi munthu iwe, mau anga onse ndidzawanena ndi iwe uwalandire m'mtima mwako, utawamva m'makutu mwako.

11. Numuke, nufike kwa andende kwa ana a anthu a mtundu wako, nunene nao ndi kuwauza, Atero Yehova Mulungu, ngakhale akamva kapena akaleka kumva.

12. Pamenepo mzimu unandinyamula, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau a mkokomo waukuru, ndi kuti, Wodala ulemerero wa Yehova m'malo mwace.

13. Ndipo ndinamva mkokomo wa mapiko a zamoyozo pakukhudzana, ndi mlikiti wa njingazo m'mbali mwa izo, ndilo phokoso la mkokomo waukuru.

14. M'mwemo mzimu unandinyamula ndi kucoka nane; ndipo ndinamuka wowawidwa, womyuka mtima; koma dzanja la Yehova linandigwirizitsa,

15. Ndipo ndinafika kwa andende ku Telabibu, okhala kumtsinje Kebara, ndiko kwao; ndipo ndinakhalako woda bwa pakati pao masiku asanu ndi awiri.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 3