Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 28:9-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Kodi udzanena ndithu pamaso pa iye wakupha iwe, Ine ndine Mulungu, pokhala uli munthu, wosati Mulungu, m'dzanja la iye wakupha iwe.

10. Udzafa mafedwe a osadulidwa ndi dzanja la alendo, pakuti ndacinena, ati Ambuye Yehova.

11. Nandidzeranso mau a Yehova, akuti,

12. Wobadwa ndi munthu iwe, kweza nyimbo ya maliro yolirira mfumu ya Turo, nuziti kwa iye, Atero Ambuye Yehova, Wakomera muyeso ndi cizindikilo, wodzala ndi nzeru wokongola wangwiro.

13. Unali m'Edene, munda wa Mulungu, mwala uli wonse wa mtengo wace unali copfunda cako, sardiyo, topazi, diamondi, berulo, sohamu, ndi yaspi, safiro, nofeki, bareketi, ndi golidi; malingaka ako ndi akazi ako anakutumikira tsiku lolengedwa iwe zinakonzekeratu.

14. Unali kerubi wodzozedwa wakuphimba, ndipo ndinakuika unali pa phiri lopatulika la Mulungu, anayendayenda pakati pa miyala yamoto.

15. Unali wangwiro m'njira zako cilengedwere iwe, mpaka cinapezeka mwa iwe cosalungama.

16. Mwa kucuruka kwa malonda ako anakudzaza m'kati mwako ndi ciwawa, ndipo unacimwa; cifukwa cace ndinakukankha kukucotsa pa phiri la Mulungu; ndipo ndinakuononga, kerubi wakuphimba iwe, kukucotsa pakati pa miyala yamoto.

17. Unadzikuza mtima cifukwa ca kukongola kwako, waipsa nzeru zako; cifukwa ca kuwala kwako ndakugwetsa pansi, ndakuika pamaso pa mafumu, kuti akupenye.

18. Mwa mphulupulu zako zocuruka ndi malonda ako osalungama waipsa malo ako opatulika; cifukwa cace ndaturutsa moto m'kati mwako wakunyeketsa iwe; ndipo ndakusandutsa mapulusa panthaka pamaso pa onse akuona.

19. Onse akudziwa iwe mwa mitundu ya anthu adzadabwa nawe; wasanduka coopsa, ndipo sudzakhalanso konse.

20. Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 28