Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 27:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,

2. Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, Takwezera Turo nyimbo ya maliro;

3. nuti kwa Turo, Iwe wakukhala polowera m'nyanja, wakucita malonda ndi mitundu ya anthu m'zisumbu zambiri, atero Ambuye Yehova, Iwe, Turo, wati, Ine ndine wokongola wangwiro.

4. M'mphepete mwako muli m'kati mwa nyanja, iwo anakumanga iwe anakonza kukongola kwako kukhale kwangwiro.

5. Anaceka matabwa ako onse amlombwa wa ku Seniri, anatenga mikungudza ya ku Lebano kukupangira milongoti.

6. Anasema nkhafi zako za thundu wa ku Basana, anapanga mipando yako yamnyanga, woika mu mtengo wanaphini wocokera ku zisumbu za Kitimu.

7. Thanga lako ndi labafuta wopikapika wa ku Aigupto, likhale ngati mbendera yako; cophimba cako ndico nsaru yamadzi ndi yofiirira zocokera ku zisumbu za Elisa.

8. Okhala m'Zidoni ndi Arivadi ndiwo opalasa ako; anzeru ako, Turo, okhala mwa iwe, ndiwo oongolera ako.

9. Akr-ru a ku Gebala ndi eni luso ace anali mwa iwe kukonza ziboo zako; zombo zonse za kunyanja pamodzi ndi amarinyero ao anali mwa iwe kusinthana nawe malonda.

10. Aperisiya, Aludi, Apuri, anali m'khamu lako; anthu ako a nkhondo anapacika cikopa ndi cisoti mwa iwe, anamveketsa kukoma kwako.

11. Anthu a Ativadi pamodzi ndi ankhondo ako anali pa malinga ako pozungulira, ndi Agamadi anali mu nsanja zako; anapacika zikopa zao pa makoma ako pozungulira, anakwaniritsa kukoma kwako.

12. Tarisi anagulana nawe malonda m'kucuruka kwa cuma ciri conse; anagula malonda ako ndi siliva ndi citsulo, seta ndi ntobvu.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 27