Thanga lako ndi labafuta wopikapika wa ku Aigupto, likhale ngati mbendera yako; cophimba cako ndico nsaru yamadzi ndi yofiirira zocokera ku zisumbu za Elisa.