Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 26:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali caka cakhumi ndi cimodzi, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,

2. Wobadwa ndi munthu iwe, popeza Turo ananyodola Yerusalemu, ndi kuti, Onyo, watyoka uwu udali cipata ca mitundu ya anthu; wanditembenukira ine; ndidzakhuta ine, wapasuka uwu;

3. cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taona ndikutsutsa iwe, Turo, ndidzakukweretsera amitundu, monga nyanja iutsa mafunde ace.

4. Ndipo adzagumula malinga a Turo, ndi kugwetsa nsanja zace; inde ndidzausesa pfumbi lace, ndi kuuyesa pathanthwe poyera.

5. Udzakhala poyanika khokapakati pa nyanja, pakuti Ine ndacinena, ati Ambuye Yehova; ndipo udzakhala cofunkha ca amitundu.

6. Ndi ana ace akazi okhala kumunda adzaphedwa ndi lupanga; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

7. Pakuti atero Ambuye Yehova, Taona ndidzafikitsira Turo Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, mfumu ya mafumu, yocokera kumpoto ndi akavalo, ndi magareta, ndi apakavalo, ndi msonkhano wa anthu ambiri.

8. Ana ako akazi adzawapha kumunda ndi lupanga; ndipo adzakumangira nsanja, ndi kukuundira mtumbira, ndi kukuimikira cikopa.

9. Nadzaikira malinga ako zogumulira, nadzagwetsa nsanja zako ndi zida zace.

10. Papeza acuruka akavalo ace, pfumbi lao lidzakukuta; malinga ako adzagwedezeka ndi phokoso la apakavalo, ndi njinga za magareta, palowa iye pa zipata zako, monga umo amalowera m'mudzi popasukira linga lace.

11. Ndi ziboda za akavalo ace iye adzapondaponda m'makwalala ako onse; adzapha anthu ako ndi lupanga; ndi zoimiritsa za mphamvu yako zidzagwa pansi.

12. Ndipo adzalanda cuma cako ndi kufunkha malonda ako, nadzagwetsa malinga ako ndi kupasula nyumba zako zofunika, nadzaponya miyala yako, ndi mitengo yako, ndi pfumbi lako, m'madzi.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 26