Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 24:9-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Tsoka mudzi wokhetsa mwazi, ndidzakulitsa mulu wa nkhuni.

10. Zicuruke nkhuni, kuleza moto, nyama ipse, uwiritse msuzi wace, ubwadamuke, ndi mafupa ace atibuke.

11. Pamenepo uukhazike pa makara ace opanda kanthu m'menemo, kuti utenthe, nuyake mkuwa wace; ndi kuti codetsa cace cisungunuke m'mwemo, kuti dzimbiri lace lithe.

12. Nchito ya mphika ndi yolemetsa, koma dzimbiri lace lalikuru siliucokera, dzimbiri lace liyenera kumoto.

13. M'codetsa cako muli dama, popeza ndinakuyeretsa; koma sunayeretsedwa, sudzayeretsedwanso kukucotsera codetsa cako, mpaka nditakwaniritsa ukali wanga pa iwe.

14. Ine Yehova ndacinena, cidzacitika; ndipo ndidzacicita, sindidzamasula, kapena kulekerera, kapena kuwaleka, monga mwa njira zako, ndi monga umo unacitira adzakuweruza iwe, ati Ambuye Yehova.

15. Mau a Yehova anandidzeranso, akuti,

16. Wobadwa ndi munthu iwe, taona, ndikucotsera cokonda maso ako ndi cikomo, koma usamve cisoni, kapena kulira, kapena kudza misozi.

17. Usa moyo mosamveka, usalira wakufayo, dzimangire cilemba, nubvale nsapato ku mapazi ako, usaphimbe milomo yako, kapena kudya mkate wa anthu.

18. Ndipo nditalankhula ndi anthu m'mawa, madzulo ace mkazi wanga anamwalira; ndi m'mawa mwace ndinacita monga anandilamulira.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 24