Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 23:14-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo anaonjeza zigololo zace, naona amuna olembedwa pakhoma, zithunzithunzi za Akasidi olembedwa ndi kundwe;

15. omangira malamba m'cuuno mwao, ndi nduwira zazikuru zonika pamitu pao, maonekedwe ao ngati akalonga onsewo, akunga a ku Babulo, dziko la kubadwa kwao ndi Kasidi.

16. Ndipo pakuwaona anawalakalaka, nawatumira mithenga ku dziko la Akasidi.

17. Namdzera a ku Babulo ku kama wa cikondi, namdetsa ndi cigololo cao, iyenso anadetsedwa nao; atatero moyo wace unafukidwa nao.

18. M'mwemo iye anaulula cigololo cace, nabvula umarisece wace; pamenepo moyo wanga unaipidwa naye, monga umo moyo unaipidwira mkuru wace.

19. Koma anacurukitsa zigololo zace, nakumbukila masiku a ubwana wace, muja anacita cigololo m'dziko la Aigupto.

20. Ndipo anaumirira amuna ao amene nyama yao ikunga ya aburu, ndi kutentha kwao ngati kutentha kwa akavalo.

21. Momwemo wautsanso coipa ca ubwana wako, pakukhudza Aaigupto nsonga za maere ako, cifukwa ca maere a ubwana wako.

22. Cifukwa cace, Oholiba, atero Ambuye Yehova, Taona ndidzakuutsira mabwenzi ako amene moyo wako wakufidwa nao, ndi kukufikitsira iwowa pozungulira ponse atsutsane nawe,

23. a ku Babulo, ndi Akasidi, Pekodi, ndi Sowa, ndi Kowa, ndi Aasuri onse pamodzi nao, anyamata ofunika, ziwanga ndi akazembe onsewo, akalonga ndi mandoda onsewo, oyenda ndi akavalo.

24. Ndipo adzakudzera ndi zida, magareta a nkhondo, ndi magareta ena, pamodzi ndi msonkhano wa mitundu ya anthu; adzadziikira pozungulira pako ndi zikopa zocinjiriza ndi zisoti; ndipo ndidzawaika aweruze, nadzakuweruza monga mwa maweruzo ao.

25. Ndipo ndidzakuikira nsanje yanga, nadzakucitira mwaukali, iwowa adzakudula mphuno ndi makutu; ndi otsiriza ako adzagwa ndi lupanga, adzakucotsera ana ako amuna ndi akazi, ndi otsirizira ako adzatha ndi moto.

26. Adzakubvulanso zobvala zako, ndi kukucotsera zokometsera zako zokongola.

27. Motero ndidzakuleketsera coipa cako, ndi cigololo cako cocokera m'dziko la Aigupto; ndipo sudzazikwezeranso maso ako, kapena kukumbukiranso Aigupto,

28. Pakuti atero Ambuye Yehova, Taona ndidzakupereka m'dzanja la iwo amene uwada, m'dzanja la iwo amene moyo wako ufukidwa nao;

29. ndipo adzacita nawe mwaudani, nadzalanda zonse udazigwirira nchito, nadzakusiya wamarisece ndi wausiwa; ndi umarisece wa zigololo zako udzabvulidwa, dama lako ndi zigololo zako zomwe.

30. Izi adzakucitira cifukwa watsata amitundu, ndi kucita nao cigololo, popezanso wadetsedwa ndi mafano ao.

31. Wayenda m'njira ya mkuru wako, cifukwa cace ndidzapereka cikho cace m'dzanja lako.

32. Atero Ambuye Yehova, M'cikho ca mkuru wako udzamweramo ndico cacikuru ngati mcenje; adzakuseka pwepwete, nadzakunyoza muli zambiri m'menemo.

33. Udzadzala ndi kuledzera ndi cisoni, ndi cikho codabwitsa ndi ca cipasuko, ndi cikho ca mkuru wako Samariya.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 23