Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 22:4-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Waparamula nao mwazi wako, waukhetsa, nudetsedwa nao mafano ako udawapanga, nuyandikizitsa masiku ako, wafikiranso zako zako; cifukwa cace ndakuika ukhale citonzo ca amitundu ndi coseketsa ca maiko onse.

5. Okhala pafupi ndi okhala patali adzakuseka pwepwete, wodetsedwa dzina iwe, wodzala ndi kusokosera.

6. Taona akalonga a Israyeli, yense monga mwa mphamvu yace, akhala mwa iwe, kuti akhetse mwazi.

7. Mwa iwe anapepula atate ndi mai, pakati pa iwe anamcitira mlendo momzunza, mwa iwe anazunza ana amasiye, ndi mkazi wamasiye.

8. Wanyoza zopatulika zanga, waipsa masabata anga.

9. Anthu oneneza anali mwa iwe, kuti akhetse mwazi; ndipo anadya pamapiri mwa iwe, pakati pa iwe anacita zamanyazi.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 22