Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 22:1-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Anandidzeransomau a Yehova, akuti,

2. Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, udzaweruza, udzauweruza mudziwo wa mwazi kodi? uudziwitse tsono zonyansa zace zonse.

3. Nuziti, Atero Ambuye Yehova, Ndiwo mudzi wokhetsa mwazi pakati pace, kuti nthawi yace ifike, nudzipangire mafano kudzidetsa nao.

4. Waparamula nao mwazi wako, waukhetsa, nudetsedwa nao mafano ako udawapanga, nuyandikizitsa masiku ako, wafikiranso zako zako; cifukwa cace ndakuika ukhale citonzo ca amitundu ndi coseketsa ca maiko onse.

5. Okhala pafupi ndi okhala patali adzakuseka pwepwete, wodetsedwa dzina iwe, wodzala ndi kusokosera.

6. Taona akalonga a Israyeli, yense monga mwa mphamvu yace, akhala mwa iwe, kuti akhetse mwazi.

7. Mwa iwe anapepula atate ndi mai, pakati pa iwe anamcitira mlendo momzunza, mwa iwe anazunza ana amasiye, ndi mkazi wamasiye.

8. Wanyoza zopatulika zanga, waipsa masabata anga.

9. Anthu oneneza anali mwa iwe, kuti akhetse mwazi; ndipo anadya pamapiri mwa iwe, pakati pa iwe anacita zamanyazi.

10. Anabvula umarisece wa atate ao mwa iwe, mwa iwe anacepsa wodetsedwa ndi kooloka kwace.

11. Ndipo wina anacita conyansa ndi mkazi wa mnansi wace, winanso wadetsa mpongozi wace mwamanyazi, ndi wina mwa iwe anaipitsa mlongo wace mwana wamkazi wa atate wace.

12. Analandira mphotho mwa iwe kukhetsa mwazi, walandira phindu loonjezerapo, wanyengerera anansi ako ndi kuwazunza, ndipo wandiiwala Ine, ati Ambuye Yehova.

13. Taona, ndaomba manja pa phindu lako lonyenga waliona, ndi pa mwazi wokhala pakati pako.

14. Mtima wako udzaimika kodi, manja ako adzalimbikira masikuwo ndidzacita nawe? Ine Yehova ndanena, ndidzacicita.

15. Ndipo ndidzakumwaza mwa amitundu, ndi kukubalalitsa m'maiko, ndi kukuthera zodetsa zako zikucokere.

16. Ndipo udzaipsidwa mwa iwe wekha pamaso pa amitundu; motero udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 22