Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 21:20-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Uiike njira yodzera lupanga kumka ku Raba wa ana a Amoni, ndi ya ku Yuda ku Yerusalemu, mudzi walinga.

21. Pakuti mfumu ya ku Babulo aima pa mphambano ya njira, polekana njira ziwirizo, kuti aombeze maula; agwedeza mibvi, afunsira kwa aterafi, apenda ndi ciwindi.

22. M'dzanja lace lamanja muli ula wa ku Yerusalemu, kuika zogundira, kutsegula pakamwa pa kupha, kukweza mau ndi kupfuula, kuikira zitseko zogundira, kuundira mtumbira, kumanga malinga.

23. Ndipo kudzakhala ngati kuombeza konyenga pamaso pa iwo amene anawalumbirira malumbiro; koma akumbutsa mphulupulu kuti akodwe.

24. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza mwakumbutsa mphulupulu yanu pobvumbuluka zolakwa zanu, kotero kuti macimo anu aoneka m'zonse muzicita, popeza mukumbukika, mudzagwidwa ndi dzanja.

25. Ndipo iwe wolasidwa woipa, kalonga wa Israyeli, amene lafika tsiku lako, nthawi ya mphulupulu yotsiriza;

26. atero Ambuye Yehova, Cotsa cilemba, bvula korona, ufumu sudzakhalanso momwemo, kweza copepuka, cepsa cokwezeka.

27. Ndidzagubuduza gubuduza gubuduza ufumu uno, sudzakhalanso kufikira akadza Iye mwini ciweruzo; ndipo ndidzaupereka kwa Iye.

28. Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, nenera, nuziti, Atero Ambuye Yehova za ana a Amoni, ndi za citonzo cao; nuziti, Lupanga, lupanga lasololedwa, latuulidwa, kuti likaphe, kuti liononge, likhale lonyezimira.

29. Akuonera zopanda pace, akuombezera mabodza, lupanga likugoneka pa makosi a oipa olasidwa, amene lafika tsiku lao nthawi ya mphulupulu yotsiriza.

30. Ulibwezere m'cimace. Pamalo unalengedwapo m'dziko la kubadwa kwako ndidzakuweruza.

31. Ndipo ndidzakutsanulira mkwiyo wanga, ndidzakuuzira ndi moto wa kuzaza kwanga, ndidzakuperekanso m'manja mwa anthu ankharwe odziwa kuononga.

32. Udzakhala ngati nkhuni ya pamoto, mwazi wako udzakhala pakati pa dziko, sudzakumbukikanso; pakuti Ine ndine Yehova ndacinena.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 21