Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 20:17-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Koma diso langa lidawaleka osawaononga, sindinawatha onse m'cipululu.

18. Ndipo ndinati kwa ana ao m'cipululu, Musamayenda m'malemba a atate anu, musawasunga maweruzo ao, kapena kudzidetsa ndi mafano ao;

19. Ine ndine Yehova Mulungu wanu, muziyenda m'malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwacita;

20. muzipatulanso masabata anga, ndipo adzakhala cizindikilo pakati pa Ine ndi inu, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

21. Koma anawo anapandukira Ine, sanayenda m'malemba anga, kapena kusunga maweruzo anga kuwacita, amene munthu akawacita adzakhala nao ndi moyo; anaipsa masabata anga; pamenepo ndinati ndidzawatsanulira ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'cipululu.

22. Koma ndinabweza dzanja langa ndi kucicita, cifukwa ca dzina langa; kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu, amene ndinawaturutsa pamaso pao. Ndinawakwezeranso dzanja langa m'cipululu,

23. kuti ndidzawabalalitsa mwa amitundu, ndi kuwamwaza m'maiko;

24. popeza sanacita maweruzo anga, koma ananyoza malemba anga, naipsa masabata anga, ndi maso ao anatsata mafano a atate ao.

25. Momwemonso ndinawapatsa malemba amene sanali abwino, ndi maweruzo osakhala nao ndi moyo;

26. ndinawadetsanso m'zopereka zao; pakuti anapititsa pamoto onse oyamba kubadwa kuti ndiwapasule; kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova.

27. Cifukwa cace wobadwa ndi munthu iwe, lankhula ndi nyumba ya Israyeli, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Mwa icinso atate anu anandicitira mwano pakundilakwira Ine.

28. Nditafika nao m'dzikolo ndinawakwezera dzanja langa kuwapatsa ilo, anapenya citunda ciri conse cacitali, ndi mtengo uli wonse wagudugudu, naphera pomwepo nsembe zao, napetekapo nsembe zao zondiputa, aponso anacita pfungo lao lokoma, nathiraponso nsembe zao zothira.

29. Pamenepo ndinanena nao, Msanje wotani uwu mumapitako? Momwemo dzina lace lichedwa Msanje, mpaka lero lino.

30. Cifukwa cace uziti kwa nyumba ya Israyeli, Atero Ambuye Yehova, Mudzidetsa kodi monga umo anacitira makolo anu? mucita cigololo kodi kutsata zonyansa zao?

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 20