Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 20:1-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali caka cacisanu ndi ciwiri, mwezi wacisanu; tsiku lakhumi la mwezi, anadza akulu ena a Israyeli kufunsira kwa Yehova, nakhala pansi iwowa pamaso panga.

2. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

3. Wobadwa ndi munthu iwe, lankhula ndi akulu a Israyeli, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Mwadza kodi kufunsira kwa Ine? Pali Ine, sindidzafunsidwa ndi inu, ati Ambuye Yehova.

4. Udzawaweruza kodi, wobadwa ndi munthu iwe? udzawaweruza? uwadziwitse zonyansa za makolo ao,

5. nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Tsiku lija ndinamsankha Israyeli, ndi kukwezera mbeu ya nyumba ya Yakobo dzanja langa, ndi kudzidziwitsa kwa iwo m'dziko la Aigupto, pakuwakwezera dzanja langa, ndi kuti, Ine ndine Yehova Mulungu wanu;

6. tsiku lomwelo ndinawakwezera dzanja langa kuwaturutsa m'dziko la Aigupto, kumka nao ku dziko ndinawazondera, moyenda mkaka ndi uci, ndilo lokometsetsa mwa maiko onse;

7. ndipo ndinanena nao, Ali yense ataye zonyansa za pamaso pace, nimusadzidetsa ndi mafano a Aigupto; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

8. Koma anapandukira Ine, osafuna kundimvera Ine, sanataya yense zonyansa pamaso pace, sanaleka mafano a Aigupto; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'dziko la Aigupto.

9. Koma ndinacicita cifukwa ca dzina langa, kuti lisadetsedwe pamaso pa amitundu amene anakhala pakati pao, amene pamaso pao ndinadzidziwitsa kwa iwo, pakuwaturutsa m'dziko la Aigupto.

10. Momwemo ndinaturuka nao m'dziko la Aigupto, ndi kulowa nao kucipululu.

11. Ndinawapatsanso malemba anga, ndi kuwadziwitsa maweruzo anga, ndiwo munthu akawacita adzakhala nao ndi moyo.

12. Ndipo ndinawapatsanso masabata anga akhale cizindikilo pakati pa Ine ndi iwo, kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.

13. Koma nyumba ya Israyeli inapaodukira Ine m'cipululu, sanayenda m'malemba anga, nanyoza maweruzo anga, amene, munthu akawacita adzakhala nao ndi moyo; ndi masabata anga anawaipsa kwambiri; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga m'cipululu kuwatha.

14. Koma ndinacicita cifukwa ca dzina langa, kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu amene ndinawaturutsa pamaso pao.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 20