Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24
  25. 25
  26. 26
  27. 27
  28. 28
  29. 29
  30. 30
  31. 31
  32. 32
  33. 33
  34. 34
  35. 35
  36. 36
  37. 37
  38. 38
  39. 39
  40. 40
  41. 41
  42. 42
  43. 43
  44. 44
  45. 45
  46. 46
  47. 47
  48. 48

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Kuitanidwa kwa Ezekieli

1. Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, khala ciriri, ndipo ndidzanena nawe.

2. Ndipo unandilowa mzimu pamene ananena nane, ndi kundiimika ndikhale ciriri; ndipo ndinamumva Iye wakunena nane.

3. Nati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, ndikutumizira kwa ana a Israyeli, kwa mitundu ya anthu opanduka, amene anapandukana nane; iwo ndi makolo ao anandilakwira mpaka lero lomwe.

4. Ndipo anawa, ndiwo acipongwe ndi ouma mtima, ndikutumiza kwa iwo; ndipo ukanene nao, Atero Yehova Mulungu.

5. Ndipo iwowa, ngakhale akamva kapena akaleka kumva, (pakuti ndiwo nyumba yopanduka,) koma adzadziwa kuti panali mneneri pakati pao.

6. Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu iwe, usawaopa, kapena kuopa mau ao; ingakhale mitungwi ndi minga ikhala ndi iwe, nukhala pakati pa zinkhanira, usaopa mau ao kapena kuopsedwa ndi nkhope zao; pakuti ndiwo nyumba yopanduka.

7. Ndipo ukanene nao mau anga, ngakhale akamva kapena akaleka kumva; pakuti iwo ndiwo opanduka.

8. Koma iwe, wobadwa ndi munthu, tamvera ici ndirikunena nawe; usakhale iwewopanduka, ngati nyumba ija yopanduka; tsegula pakamwa pako, nudye comwe ndikupatsa.

9. Ndipo pakupenya ine ndinaona dzanja londiturutsira, ndipo taonani, mpukutu wa buku m'mwemo;

10. naufunyulula pamaso panga; ndipo unalembedwa m'kati ndi kubwalo; munalembedwa m'mwemo nyimbo za maliro, ndi cisoni, ndi tsoka.