Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24
  25. 25
  26. 26
  27. 27
  28. 28
  29. 29
  30. 30
  31. 31
  32. 32
  33. 33
  34. 34
  35. 35
  36. 36
  37. 37
  38. 38
  39. 39
  40. 40
  41. 41
  42. 42
  43. 43
  44. 44
  45. 45
  46. 46
  47. 47
  48. 48

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Mtengo wopanda pace

1. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

2. Wobadwa ndi munthu iwe, mtengo wampesa uposeranji mtengo uli wonse wina, nthambi ya mpesa yokhalayo mwa mitengo ya kunkhalango?

3. Kodi atengako mtengo kupanga nao nchito? atengako ciciri kodi kupacikapo cipangizo ciri conse?

4. Taona, auponya kumoto kuuyesa nkhuni, moto unyeketsa nsonga zace zonse ziwiri, nupserera pakati pace, kodi ukomera nchito Irf yonse?

5. Taonani, pokhala wamphumphu sunayenera nchito iri yonse, nanga utanyeketsa moto nupserera udzayeneranso nchito iri yonse?

6. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Ngati mtengo wampesa pakati pa mitengo ya kunkhalango ndauponya kumoto ukhale nkhuni, momwemo ndidzapereka okhala m'Yerusalemu.

7. Ndipo ndidzaika nkhope yanga iwatsutse; adzaturuka kumoto, koma moto udzawatha; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuika Ine nkhope yanga iwatsutse.

8. Ndipo ndidzasandutsa dziko cipululu; popeza anacita colakwa, ati Ambuye Yehova.