Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 17:14-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. kuti ufumuwo ukhale wopepuka, kuti usadzikweze, koma kuti pakusunga pangano lace ukhale.

15. Koma anapandukira ndi kutuma mithenga yace ku Aigupto, kuti ampatse akavalo ndi anthu ambiri. Adzapindula kodi? adzapulumuka wakucita izi? atyole pangano ndi kupulumuka kodi?

16. Pali Ine, ati Ambuye Yehova, pamalo pokhala mfumu, imene idamcititsa ufumu, imene anapeputsa lumbiro lace, imene anatyola pangano lace, adzafa pamodzi ndi iye pakati pa Babulo.

17. Ndipo Farao ndi nkhondo yace yaikuru, ndi khamu lace launyinji, sadzacita pamodzi naye kunkhondo, pakuunda mtumbira, ndi kumanga malinga, kulikha anthu ambiri.

18. Pakuti anapepula lumbiro, ndi kutyola pangano, angakhale anapereka dzanja lace; popeza anacita izi zonse sadzapulumuka.

19. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Pali Ine, lumbiro langa, analipepula, ndi pangano langa analityola, ndidzawabweza pamutu pace.

20. Ndidzamphimbanso ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzadza naye ku Babulo, ndi kunena naye komweko mlandu wa kulakwa kwace anandilakwira nako.

21. Ndipo othawa ace onse m'magulu ace onse adzagwa ndi lupanga, ndi otsala adzabalalitsidwa ku mphepo zonse; ndipo mudzadziwa kuti Ine Yehova ndanena.

22. Atero Ambuye Yehova, Ndidzatenganso nsonga ya mkungudza wautali ndi kulika; ndidzabudula nsonga yosomphoka'ya nthambi zace zanthete, ndi kuioka pa phiri lalitali lothubvuka;

23. pa phiri lothubvuka la Israyeli ndidzaioka, ndipo idzaphuka nthambi ndi kubala zipatso, nidzakhala mkungudza wokoma, ndi m'munsi mwace mudzakhala mbalame ziri zonse za mapiko ali onse; mu mthunzi wa nthambi zace zidzabindikira.

24. Ndipo mitengo yonse ya kuthengo idzadziwa kuti Ine Yehova ndatsitsa mtengo wosomphoka, ndakuza mtengo waung'ono, ndaumitsa mtengo wauwisi, ndi kuphukitsa mtengo wouma; Ine Yehova ndanena ndi kucicita.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 17