Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 12:13-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndidzamphimba ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzafika naye ku Babulo, ku dziko la Akasidi; sadzaliona, cinkana adzafako.

14. Ndipo onse omzinga kumthandiza, ndi magulu ace onse, ndidzawamwaza ku mphepo zonse, ndidzawasololeranso lupanga lakuwatsata.

15. Motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuwamwaza Ine mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko.

16. Koma ndidzawasiya owerengeka apulumuke lupanga, ndi njala, ndi mliri, kuti afotokoze zonyansa zao kwa amitundu kumene afikako; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

17. Anandidzeranso mau a Mulungu, akuti,

18. Wobadwa ndi munthu iwe, udye mkate wako ndi kunthunthumira, ndi kumwa madzi ako ndi kunjenjemera, ndi kutenga nkhawa;

19. nunene kwa anthu a m'dziko, Atero Yehova Mulungu za iwo okhala m'Yerusalemu, ndi za dziko la Israyeli, Adzadya mkate wao ndi nkhawa, ndi kumwa madzi ao ndi kusumwa; pakuti dziko lao lidzakhala lacipululu, kuleka kudzala kwace cifukwa ca ciwawa ca onse okhalamo.

20. Ndi midzi yokhalamo anthu idzapasuka, ndi dziko lidzakhala labwinja; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

21. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

22. Wobadwa ndi munthu iwe, ngwotani mwambi umene muli nao m'dziko la Israyeli, wakuti, Masiku acuruka, ndi masomphenya ali onse apita pacabe?

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 12