Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 12:10-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Unene nao, Atero Ambuye Yehova, Katundu uyu anena za kalonga wa m'Yerusalemu, ndi nyumba yonse ya Israyeli yokhala pakati pao.

11. Uziti, Ine ndine cizindikilo canu, monga ndacita ine momwemo kudzacitidwa nao; adzacotsedwa kumka kundende.

12. Kalongayo ali pakati pao adzasenza paphewa pace mumdima, nadzaturuka; adzaboola palinga, nadzaturutsapo; adzaphimba nkhope yace kuti asapenye dziko ndi maso ace.

13. Ndidzamphimba ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzafika naye ku Babulo, ku dziko la Akasidi; sadzaliona, cinkana adzafako.

14. Ndipo onse omzinga kumthandiza, ndi magulu ace onse, ndidzawamwaza ku mphepo zonse, ndidzawasololeranso lupanga lakuwatsata.

15. Motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuwamwaza Ine mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko.

16. Koma ndidzawasiya owerengeka apulumuke lupanga, ndi njala, ndi mliri, kuti afotokoze zonyansa zao kwa amitundu kumene afikako; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 12