Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 1:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. NDIPO kunali caka ca makumi atatu, mwezi wacinai, tsiku lacisanu la mwezi, pokhala ine pakati pa andende kumtsinje Kebara, kunatseguka kumwamba, ndipo ndinaona masomphenya a Mulungu.

2. Tsiku lacisanu la mwezi, ndico caka cacisanu ca kutengedwa ndende mfumu Yoyakini,

3. anadzadi mau a Yehova kwa Ezekieli wansembe, mwana wa Buzi, m'dziko la Akasidi kumtsinje Kebara; ndi pomwepo dzanja la Yehova lidamkhalira.

4. Ndinapenya, ndipo taonani, mkuntho wa mphepo wocokera kumpoto, mtambo waukuru ndi moto wopfukusika m'mwemo, ndi pozungulira pace padacita ceza, ndi m'kati mwace mudaoneka ngati citsulo cakupsa m'kati mwa moto.

5. Ndi m'kati mwace mudaoneka mafaniziro a zamoyo zinai. Ndipo maonekedwe ao ndiwo anafanana ndi munthu,

6. ndi yense anali nazo nkhope zinai, ndi yense wa iwo anali nao mapiko anai.

7. Ndi mapazi ao anali mapazi oongoka, ndi ku mapazi ao kunanga kuphazi kwa mwana wa ng'ombe; ndipo ananyezimira ngati mawalidwe a mkuwa wowalitsidwa.

8. Zinali naonso manja a munthu pansi pa mapiko ao pa mbali zao zinai; ndipo zinaizi zinali nazo nkhope zao ndi mapiko ao.

9. Mapiko ao analumikizana; sizinatembenuka poyenda; ciri conse cinayenda ndi kulunjika kutsogoloko.

10. Mafaniziro a nkhope zao zinali nayo nkhope ya munthu; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya mkango pa mbali ya ku dzanja lamanja; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya ng'ombe pa mbali ya ku dzanja lamanzere; izi zinai zinali nayonso nkhope ya ciombankhanga.

11. Ndi nkhope zao ndi mapiko ao zinagawikana kumutu; ciri conse cinali nao mapiko awiri olumikizana, ndi awiri anaphimba thupi.

12. Ndipo zinayenda, ciri conse cinalunjika kutsogolo kwace uko mzimu unafuna kumukako zinamuka, sizinatembenuka poyenda.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 1