Ndinapenya, ndipo taonani, mkuntho wa mphepo wocokera kumpoto, mtambo waukuru ndi moto wopfukusika m'mwemo, ndi pozungulira pace padacita ceza, ndi m'kati mwace mudaoneka ngati citsulo cakupsa m'kati mwa moto.