Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezara 7:8-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo iye anafika ku Yerusalemu mwezi wacisanu, ndico caka cacisanu ndi ciwiri ca mfumu.

9. Pakuti tsiku loyamba la mwezi woyamba, ndilo ciyambi ca ulendo wokwera kucokera ku Babulo, ndi tsiku lacimodzi la mwezi wacisanu anafika ku Yerusalemu, monga linamkhalira dzanja lokoma la Mulungu wace.

10. Pakuti Ezara adaikiratu mtima wace kucifuna cilamulo ca Yehova, ndi kucicita, ndi kuphunzitsa m'Israyeli malemba ndi maweruzo.

11. Malemba a kalatayo mfumu Aritasasta anampatsa Ezara wansembe mlembi, ndiye mlembi wa mau a malamulo a Yehova, ndi malemba ace kwa Israyeli, ndi awa:

12. Aritasasta mfumu ya mafumu kwa Ezara wansembe, mlembi wa lamulo la Mulungu wa Kumwamba, mtendere weni weni, ndi pa nthawi yakuti.

Werengani mutu wathunthu Ezara 7