Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezara 7:24-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Tikudziwitsaninso kuti sikudzaloledwa kusonkhetsa ali yense wa ansembe, ndi Alevi, oyimbira, odikira, Anetini, kapena anchito a nyumba iyi ya Mulungu msonkho, thangata, kapena msonkho wa panjira.

25. Ndipo iwe Ezara monga mwa nzeru za Mulungu wako iri m'dzanja lako, uike nduna, ndi oweruza mirandu, aweruze anthu onse ali tsidya lija la mtsinje, onse akudziwa malamulo a Mulungu wako; ndi wosawadziwayo umphunzitse.

26. Ndipo ali yense wosacita lamulo la Mulungu wako, ndi lamulo la mfumu, mlandu umtsutse msanga, ngakhale kumupha, kapena kumpitikitsa m'dziko, kapena kumlanda cuma cace, kapena kummanga m'kaidi.

27. Wodala Yehova Mulungu wa makolo athu, amene anaika cinthu cotere mu mtima wa mfumu, kukometsera nyumba ya Yehova iri ku Yerusalemu,

28. nandifikitsira cifundo pamaso pa mfumu, ndi aphungu ace, ndi pamaso pa akalonga amphamvu onse a mfumu. Motero ndinalimbika mtima, monga umo dzanja la Yehova Mulungu wanga linakhala pa ine; ndipo ndinasonkhanitsa mwa Israyeli anthu omveka akwere nane limodzi.

Werengani mutu wathunthu Ezara 7