Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezara 6:15-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Nitsirizidwa nyumba iyi tsiku lacitatu la mwezi wa Adara, ndico caka cacisanu ndi cimodzi ca ufumu wa Dariyo mfumu.

16. Ndipo ana a Israyeli, ansembe ndi Alevi, ndi ana otsala a ndende, anapereka nyumba iyi ya Mulungu mokondwera.

17. Ndipo popatulira nyumba iyi ya Mulungu anapereka ng'ombe zana limodzi, nkhosa zamphongo mazana awiri, ana a nkhosa mazana anai, ndi za nsembe yazolakwa ya Aisrayeli onse atonde khumi ndi awiri, monga mwa kuwerenga kwace kwa mapfuko a Israyeli.

18. Naika ansembe m'magawo mwao, ndi Alevi m'magawidwe mwao, atumikire Mulungu wokhala ku Yerusalemu, monga mulembedwa m'buku la Mose.

19. Ndipo ana a ndende anacita Paskha tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi woyamba.

20. Pakuti ansembe ndi Alevi anadziyeretsa pamodzi, anayera onsewo, naphera Paskha cifukwa ca ana onse a ndende, ndi abale ao ansembe, ndi iwo okha.

21. Ndipo ana a Israyeli obwera kundende, ndi yense wakudzipatulira kucokera conyansa ca amitundu, kutsata iwowa, kufuna Yehova Mulungu wa Israyeli, anadza,

22. nasunga madyerero a mkate wopanda cotupitsa masiku asanu ndi awiri ndi cimwemwe; pakuti Yehova adawakondweretsa, nawatembenuzira mtima wa mfumu ya Asuri, kulimbitsa manja ao mu nchito ya nyumba ya Mulungu, Mulungu wa Israyeli.

Werengani mutu wathunthu Ezara 6