Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezara 4:12-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Adziwe mfumu kuti, Ayuda adakwerawo ocokera kwanu atifikira ife ku Yerusalemu, alikumanga mudzi uja wopanduka ndi woipa, alikutsiriza malinga ace, nalumikiza maziko ace.

13. Adziwe tsono mfumu, kuti akamanga mudzi uwu ndi kutsiriza malinga ace, sadzapereka msonkho, kapena thangata, kapena msonkho wa m'njira; ndipo potsiriza pace kudzasowetsa mafumu.

14. Popeza tsono timadya mcere wa m'nyumba ya mfumu, sitiyenera kungopenyerera mpepulo wa pa mfumu; cifukwa cace tatumiza ndi kudziwitsa mfumu,

15. kuti afunefune m'buku la cikumbutso la makolo anu; momwemo mudzapeza m'buku la cikumbutso, ndi kudziwa kuti mudzi uwu ndi mudzi wopanduka, ndi wosowetsa mafumu, ndi maiko; ndi kuti amadziyendera m'menemo kuyambira kale lomwe; ndico cifukwa cakuti anapasula mudzi uwu.

16. Tirikudziwitsa mfumu kuti ukamangidwa mudziwu, nakatsirizidwa malinga ace, simudzakhala nalo gawo tsidya lino la mtsinjewo.

17. Mfumu nibweza mau kwa Rehumu ciwinda ca malamulo, ndi kwa Simsai mlembi, ndi kwa anzao otsala okhala m'Samariya, ndi otsala tsidya lino la mtsinjewo, Mtendere, ndi nthawi yakuti.

18. Kalatayo mwatitumizira anandiwerengera momveka.

19. Ndipo ndinalamulira anthu, nafunafuna, napeza kuti mudzi uwu unaukira mafumu kuyambira kale lomwe ndi kuti akacitamo mpanduko ndi kudziyendera.

20. Panalinso mafumu amphamvu m'Yerusalemu amene anacita ufumu tsidya lija lonse la mtsinje, ndipo anthu anawapatsa msonkho, thangata, ndi msonkho wa m'njira.

21. Mulamulire tsono kuti anthu awa aleke, ndi kuti asamange mudzi uwu, mpaka ndidzalamulira ndine.

22. Cenjerani mungadodomepo, cidzakuliranji cisauko ca kusowetsa mafumu?

23. Pamenepo atawerenga malemba a kalata wa mfumu kwa Rehumu, ndi Simsai mlembi, ndi anzao, anafulumira kupita ku Yerusalemu kwa Ayuda, nawaletsa ndi dzanja lamphamvu.

24. Momwemo inalekeka nchito ya nyumba ya Mulungu yokhala ku Yerusalemu; nilekeka mpaka caka caciwiri ca ufumu wa Dariyo mfumu ya Perisiya.

Werengani mutu wathunthu Ezara 4