Mfumu nibweza mau kwa Rehumu ciwinda ca malamulo, ndi kwa Simsai mlembi, ndi kwa anzao otsala okhala m'Samariya, ndi otsala tsidya lino la mtsinjewo, Mtendere, ndi nthawi yakuti.