Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezara 10:15-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Yonatani mwana wa Asaheli ndi Yazeya mwana wa Tikiva okha anatsutsana naco, ndi Mesulamu ndi Sabetai Mlevi anawathandiza.

16. Pamenepo anthu otengedwa ndende anacita cotero. Ndi Ezara wansembe, ndi anthu akuru a nyumba za makolo, monga mwa nyumba za makolo ao, iwo onse ochulidwa maina ao anasankhidwa, nakhala pansi tsiku loyamba la mwezi wakhumi kufunsa za mlanduwu.

17. Natsiriza nao amuna onse adadzitengera akazi acilendo tsiku loyamba la mwezi woyamba.

18. Ndipo anapeza mwa ana a ansembe odzitengera akazi acilendo, ndiwo a ana a Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ace Maseya, ndi Eliezere, ndi Yaribu, ndi Gedaliya.

19. Ndipo anaimika dzanja lao kuti adzacotsa akazi ao; ndipo popeza adaparamuladi, anapereka nsembe nkhosa yamphongo ya zoweta pa kuparamula kwao.

20. Ndi a ana a Imeri: Hanani ndi Zebadiya.

21. Ndi a ana a Harimu: Maseya, ndi Eliya, ndi Semaya, ndi Yehiyeli, ndi Uziya.

22. Ndi a ana a Pasuru: Elioenai, Maseya, Ismayeli, Netaneli, Yozabadi, ndi. Elasa.

23. Ndi a Alevi: Yozabadi, ndi Simei, ndi Kelaya (ndiye Kelita), Petahiya, Yuda, ndi Eliezere.

24. Ndi a oyimbira: Eliasibu; ndi a odikira: Salumu, ndi Telemu, ndi Uri.

25. Ndi Aisrayeli a ana a Parosi: Ramiya, ndi Iziya, ndi Matikiya, ndi Miyamini, ndi Eleazara, ndi Malikiya, ndi Benaya.

Werengani mutu wathunthu Ezara 10