Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 9:18-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Koma Ayuda okhala m'Susani anasonkhana tsiku lace lakhumi ndi citatu ndi lakhumi ndi cinai, ndi pa tsiku lakhumi ndi cisanu anapumula, naliyesa tsiku lamadyerero ndi lakukondwera.

19. Cifukwa cace Ayuda a kumiraga, okhala m'midzi yopanda malinga, amaliyesa tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi wa Adara tsiku la kukondwera ndi madyerero, ndi tsiku lokoma, ndi lakutumizirana magawo.

20. Ndipo Moredekai analembera izi, natumiza akalata kwa Ayuda onse okhala m'maiko onse a mfumu Ahaswero, a kufupi ndi a kutali,

21. kuwalimbikitsira, asunge tsiku lakhumi ndi cinai, mwezi wa Adara, ndi tsiku lace lakhumi ndi cisanu lomwe, caka ndi caka,

22. ndiwo masiku amene Ayuda anapumula pa adani ao; ndi mwezi wacisoni unawasandulikira wakukondwera, ndi wamaliro ukhale tsiku lokoma, awayese masiku amadyerero ndi akukondwera, akutumizirana magawo, ndi akupatsa zaufulu kwa osauka.

23. Ndipo Ayuda anabvomereza kucita monga umo adayambira, ndi umo Moredekai adawalembera;

24. popeza Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, mdani wa Ayuda onse, adapangira Ayuda ciwembu kuwaononga, naombeza Puri, ndiwo ula, kuwatha ndi kuwaononga;

25. koma pofika mlanduwo kwa mfumu, anati mwa akalata kuti ciwembu cace coipa adacipangira Ayuda, cimbwerere mwini; ndi kuti Iye ndi ana amuna ace apacikidwe pamtengo,

26. Cifukwa cace anacha masikuwa Purimu, ndilo dzina la ulawo. Momwemo, cifukwa ca mau onse a kalatayo, ndi izi adaziona za mlanduwo, ndi ici cidawadzera,

27. Ayuda anakhazikitsa ici, nadzilonjezetsa okha, ndi mbeu yao, ndi onse akuphatikana nao, cingalekeke, kuti adzasunga masiku awa awiri monga mwalembedwa, ndi monga mwa nyengo yao yoikika, caka ndi caka;

28. ndi kuti masikuwa adzakumbukika ndi kusungika mwa mibadwo yonse, banja liri lonse, dziko liri lonse, ndi mudzi uli wonse; ndi kuti masiku awa sadzalekeka mwa Ayuda, kapena kusiyidwa cikumbukilo cao mwa mbeu yao.

29. Pamenepo Estere mkazi wamkuru mwana wa Abihaili, ndi Moredekai Myuda, analembera molamulira, kukhazikitsa kalata uyu waciwiri wa Purimu.

30. Natumiza iye akalata kwa Ayuda onse, ku maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri a ufumu wa Ahaswero, ndiwo mau a mtendere ndi coonadi;

Werengani mutu wathunthu Estere 9