Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 7:6-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Nati Estere, Munthu wosautsa ndi mdani ndiye Hamani woipa uyu. Pamenepo Hamani anagwidwa mantha pamaso pa mfumu ndi mkazi wamkuru.

7. Ninyamuka mfumu mu mkwiyo wace ku madyerero a vinyo, nimka ku munda wa maluwa wa kucinyumba; koma Hamani anatsalira kudzipempherera moyo kwa mkazi wamkuru Estere; popeza anapenya kuti mfumu inatsimikiza mtima kumcitira coipa.

8. Nibwera mfumu ku munda wa maluwa wa kucinyumba kulowanso m'nyumba munali madyerero a vinyo, napeza Hamani atagwa pa kama wokhalapo Estere. Niti mfumu, Kodi aumiriza mkazi wamkuru pamaso panga m'nyumba? Poturuka mau pakamwa pa mfumu anamphimba Hamani nkhope.

9. Nati Haribona wina wa adindo okhala pamaso pa mfumu, Taonaninso, mtengowo msinkhu wace mikono makumi asanu, umene Hamani anaupangira Moredekai wonenera mfumu zokoma, uimiritsidwa m'nyumba ya Hamani. Niti mfumu, Mpacike pomwepo.

10. Nampacika Hamani pa mtengo adaukonzera Moredekai. Pamenepo mkwiyo wa mfumu unatsika.

Werengani mutu wathunthu Estere 7