Ninyamuka mfumu mu mkwiyo wace ku madyerero a vinyo, nimka ku munda wa maluwa wa kucinyumba; koma Hamani anatsalira kudzipempherera moyo kwa mkazi wamkuru Estere; popeza anapenya kuti mfumu inatsimikiza mtima kumcitira coipa.