Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 7:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Motero inadza mfumu ndi Hamani kumwa naye mkazi wamkuru Estere.

2. Nitinso mfumu kwa Estere tsiku laciwirili pa madyerero a vinyo, Pempho lanu nciani, mkazi wamkuru Estere? lidzapatsidwa kwa inu; mufunanji? cidzacitika, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumu wanga.

3. Nayankha mkazi wamkuru Estere, nati, Ngati mwandikomera mtima, mfumu, ndipo cikakomera mfumu, andilekere moyo wanga pa kupempha kwanga, ndi wa anthu a mtundu wanga pa pempho langa;

4. pakuti tagulitsidwa; ine ndi anthu amtundu wanga, kuti ationonge, atiphe, natipulule, Koma tikadagulitsidwa tikhale akapolo ndi adzakazi, ndikadakhala cete; cinkana wosautsa sakadakhoza kubwezera kusowa kwa mfumu.

5. Pamenepo mfumu Ahaswero inalankhula, niti kwa mkazi wamkuru Estere, Ndani uyu, ali kuti iyeyu wadzazidwa mtima wace kuti azitero?

6. Nati Estere, Munthu wosautsa ndi mdani ndiye Hamani woipa uyu. Pamenepo Hamani anagwidwa mantha pamaso pa mfumu ndi mkazi wamkuru.

Werengani mutu wathunthu Estere 7