Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 6:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Usiku uja tulo tidamwazikira mfumu, niti abwere nalo buku la mbiri, naliwerenga pamaso pa mfumu.

2. Napeza mudalembedwa kuti Moredekai adaulula za Bigitana ndi Teresi, awiri a adindo a mfumu osunga pakhomo, amene adayesa kumthira manja mfumu Ahaswero.

3. Niti mfumu, Anamcitira Moredekai ulemu ndi ukulu wotani cifukwa ca ici? Ndipo anyamata a mfumu akuitumikira ananena nayo, Sanamcitira kanthu.

4. Niti mfumu, Ali kubwalo ndani? Koma Hamani adalowa m'bwalo lakunja la nyumba ya mfumu kulankhula ndi mfumu za kupacika Moredekai pamtengo adaukonzeratu.

5. Ndipo anyamata a mfumu ananena nayo, Taonani, Hamani alikuima pabwalo. Niti mfumu, Alowe.

6. Nalowa Hamani. Ndipo mfumu inati kwa iye, Kodi amcitire ciani munthu amene mfumu ikondwera kumcitira ulemu? Ndipo Hamani anati mumtima mwace, Ndaniyo mfumu ikondwera kumcitira ulemu koposa ine?

Werengani mutu wathunthu Estere 6