Nalowa Hamani. Ndipo mfumu inati kwa iye, Kodi amcitire ciani munthu amene mfumu ikondwera kumcitira ulemu? Ndipo Hamani anati mumtima mwace, Ndaniyo mfumu ikondwera kumcitira ulemu koposa ine?