Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 5:8-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. ngati mfumu indikomera mtima, ngatinso cakomera mfumu kupereka pempho langa ndi kucita cofuna ine, adze mfumu ndi Hamani ku madyerero ndidzawakonzera; ndipo mawa ndidzacita monga yanena mfumu.

9. Ndipo Hamani anaturuka tsiku lomwelo wosekerera ndi wokondwera mtima; koma pamene Hamani anapenya Moredekai ku cipata ca mfumu, osamnyamukira kapena kumfumukira, Hamani anadzazidwa ndi mkwiyo pa Moredekai.

10. Koma Hamani anadziletsa, namuka kwao, natumiza munthu kukatenga mabwenzi ace, ndi Zeresi mkazi wace.

11. Nawawerengera Hamani kulemera kwace kwakukuru, ndi ana ace ocuruka, ndi zonse mfumu idamkuza nazo, ndi umo adamkweza koposa akalonga ndi anyamata a mfumu.

12. Hamani anatinso, Ndiponso Estere mkazi wamkuru sanalola mmodzi yense alowe pamodzi ndi mfumu ku madyerero adakonzawo, koma ine ndekha; nandiitana mawanso pamodzi ndi mfumu.

13. Koma zonsezi sindipindula nazo kanthu konse, pokhala ndirikuona Moredekai Myudayo alikukhala ku cipata ca mfumu.

14. Pamenepo Zeresi mkazi wace, ndi mabwenzi ace onse ananena naye, Apange mtengo, msinkhu wace mikono makumi asanu, ndi mawa mukanene nayo mfumu kuti ampacike Moredekai pamenepo; nimulowe pamodzi ndi mfumu kumadyerero wokondwera. Ndipo ici cidakomera Hamani, napangitsa anthu mtengowo.

Werengani mutu wathunthu Estere 5